Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 1:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi za mapwando anu mtima wanga uzida; zindibvuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.

15. Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pocurukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.

16. Sambani, dziyeretseni; cotsani macitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kucita zoipa;

17. phunzirani kucita zabwino; funani ciweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.

18. Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu ziri zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale ziri zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.

19. Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,

20. koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; cifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.

21. Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! wodzala ciweruzowo! cilungamo cinakhalamo koma tsopano ambanda.

22. Siliva wako wasanduka mphala, vinyo wako wasanganizidwa ndi madzi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 1