Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 9:4-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Mucenjere naye yense mnansi wace, musakhulupirire yense mbale wace; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.

5. Ndipo yense adzanyenga mnansi wace, osanena coonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kucita zoipa.

6. Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.

7. Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzacitanji, cifukwa ca mwana wamkazi wa anthu anga?

8. Lilime lao ndi mubvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wace pakamwa pace, koma m'mtima mwace amlalira.

9. Kodi sindidzawalanga cifukwa ca izi? ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera cilango mtundu wotere?

10. Cifukwa ca mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, cifukwa ca mabusa a cipululu ndidzacita maliro, cifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.

11. Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.

12. Wanzeru ndani, kuti adziwe ici? ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti acilalikire? cifukwa cace dziko litha ndi kupserera monga cipululu, kuti anthu asapitemo?

13. Ndipo Yehova ati, Cifukwa asiya cilamulo canga ndinaciika pamaso pao, ndipo sanamvera mau anga, osayenda m'menemo;

14. koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa;

15. cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa civumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.

16. Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwa; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.

17. Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ocenjera, kuti adze;

18. afulumire, atikwezere ife mau a maliro, kuti maso athu agwe misozi, ndi zikope zathu ziyendetse madzi.

19. Pakuti mau a kulira amveka m'Ziyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu.

20. Koma imvani mau a Yehova, akazi inu, khutu lanu lilandire mau a pakamwa pace, phunzitsani ana anu akazi kulira, ndi yense aphunzitse mnzace maliridwe ace.

21. Pakuti imfa yakwera m'mazenera athu, yalowa m'nyumba mwathu; kucotsa ana kubwalo, ndi: anyamata kumiseu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 9