Wanzeru ndani, kuti adziwe ici? ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti acilalikire? cifukwa cace dziko litha ndi kupserera monga cipululu, kuti anthu asapitemo?