Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 9:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa;

15. cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa civumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.

16. Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwa; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.

17. Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ocenjera, kuti adze;

18. afulumire, atikwezere ife mau a maliro, kuti maso athu agwe misozi, ndi zikope zathu ziyendetse madzi.

19. Pakuti mau a kulira amveka m'Ziyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu.

20. Koma imvani mau a Yehova, akazi inu, khutu lanu lilandire mau a pakamwa pace, phunzitsani ana anu akazi kulira, ndi yense aphunzitse mnzace maliridwe ace.

21. Pakuti imfa yakwera m'mazenera athu, yalowa m'nyumba mwathu; kucotsa ana kubwalo, ndi: anyamata kumiseu.

22. Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga cipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wocitola.

23. Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zace, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yace, wacuma asadzitamandire m'cuma cace;

24. koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakucita zokoma mtima, ciweruziro, ndi cilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati. Yehova.

25. Taonani, masiku alikudza, ati Yehova, kuti ndidzalanga onse odulidwa m'kusadulidwa kwao;

26. Aigupto, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Moabu, ndi onse ometa m'mphepete mwa tsitsi lao, okhala m'cipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israyeli iri Yosadulidwa m'mtima.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 9