Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 52:3-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pakuti zonse zinacitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda cifukwa ca mkwiyo wa Yehova, mpaka anawacotsa pamaso pace; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babulo.

4. Ndipo panaoneka caka cacisanu ndi cinai ca ufumu wace mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anafika, iye ndi nkhondo yace, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zitando; ndipo anammangira malinga pozungulira pace.

5. Ndipo mudzi unazingidwa mpaka caka ca khumi ndi cimodzi ca mfumu Zedekiya.

6. Mwezi wacinai, tsiku lacisanu ndi cinai la mwezi, njala inabvuta m'mudzi, ndipo anthu a m'dziko analibe zakudya.

7. Pamenepo anaboola mudzi, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, naturuka m'mudzi usiku pa njira ya kucipata ca pakati pa makoma awiri, imene inali pa munda wa mfumu; Akasidi alikumenyana ndi mudzi pozungulira pace, ndipo anapita njira ya kucidikha.

8. Koma nkhondo ya Akasidi inamtsata mfumu, nimpeza Zedekiya m'zidikha za ku Yeriko; ndipo nkhondo yace yonse inambalalikira iye.

9. Ndipo anamgwira iye, namtengera kwa mfumu ya ku Babulo ku Ribila m'dziko la Hamati; ndipo iye anamweruza.

10. Ndipo mfumu ya ku Babulo inapha ana a Zedekiya pamaso pace; niphanso akuru onse a Yuda m'Ribila.

11. Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, ndipo mfumu ya ku Babulo inammanga m'zigologolo, nimtengera ku Babulo, nimuika m'ndende mpaka tsiku la kufa kwace.

12. Mwezi wacisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndico caka cakhumi ndi cisanu ndi cinai ca Nebukadirezara, mfumu ya ku Babulo, analowa m'Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babulo:

13. ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za m'Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikuru zonse, anazitentha ndi moto.

14. Ndipo nkhondo yonse ya Akasidi, imene inali ndi kapitao wa alonda, inagumula makoma onse a Yerusalemu pomzungulira pace.

15. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m'mudzi, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babulo, ndi otsala a unyinjiwo.

16. Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m'minda.

17. Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Akasidi anazityolatyola, nanka nao mkuwa wace wonse ku Babulo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 52