Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 51:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo ndidzatuma ku Babulo alendo, amene adzamkupira iye, amene adzataya zonse m'dziko lace, pakuti tsiku la cisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pace.

3. Wauta asakoke uta wace, asadzikweze m'malaya ace acitsulo; musasiye anyamata ace; muononge ndithu khamu lace lonse.

4. Ndipo adzagwa ophedwa m'dziko la Akasidi, opyozedwa m'miseu yace.

5. Pakuti Israyeli ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi ucimo kucimwira Woyera wa Israyeli.

6. Thawani pakati pa Babulo, yense apulumuke moyo wace; musathedwe m'coipa cace; pakuti ndi nthawi ya kubwezera cilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yace.

7. Babulo wakhala cikho cagolidi m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wace; cifukwa cace amitundu ali ndi misala.

8. Babulo wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zace bvunguti, kapena angacire.

9. Tikadaciritsa Babulo koma sanacire; mumsiye iye, tipite tonse yense ku dziko lace; pakuti ciweruziro cace cifikira kumwamba, cinyamulidwa mpaka kuthambo,

10. Yehova waturutsa cilungamo cathu; tiyeni tilalikire m'Ziyoni nchito ya Yehova Mulungu wathu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 51