Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 50:29-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Memezani amauta amenyane ndi Babulo, onse amene akoka uta; mummangire iye zitando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wace yense; mumbwezere iye monga mwa nchito yace; monga mwa zonse wazicita, mumcitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israyeli.

30. Cifukwa cace anyamata ace adzagwa m'miseu yace, ndi anthu ankhondo ace onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova.

31. Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe.

32. Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'midzi yace, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye.

33. Yehova wa makamu atero: Ana a Israyeli ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula.

34. Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lace Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumitse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babulo.

35. Lupanga liri pa Akasidi, ati Yehova, pa okhala m'Babulo, pa akuru ace, ndi pa anzeru ace.

36. Lupanga liri pa amatukutuku, ndipo adzapusa; lupanga liri pa anthu olimba ace, ndipo adzaopa.

37. Lupanga liri pa akavalo ao, ndi pa magareta ao, ndi pa anthu onse osanganizidwa amene ali pakati pace, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga liri pa cuma cace, ndipo cidzalandidwa.

38. Cirala ciri pa madzi ace, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaruka ndi kufuna zoopsa.

39. Cifukwa cace zirombo za kucipululu ndi mimbulu zidzakhalamo, ndi nthiwatiwa zidzakhala m'menemo; ndipo sadzakhalamo anthu konse; ndipo sadzakhalamo m'mibadwo mibadwo.

40. Monga muja Yehova anagwetsa Sodomu ndi Gomora ndi midzi Inzace, ati Yehova; anthu sadzakhalamo, mwana wa munthu sadzagonamo.

41. Taonani, anthu acokera kumpoto; ndiwo mtundu waukuru, ndipo mafumu ambiri adzaukitsidwa kucokera ku malekezero a dziko lapansi.

42. Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe cifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, ndipo akwera akavalo, yense aguba monga munthu wa kunkhondo, kukamenyana ndi iwe, mwana wamkazi wa Babulo.

43. Mfumu ya ku Babulo yamva mbiri yao, ndipo manja ace alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala.

44. Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wocokera ku Yordano wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umcokere, ndipo ali yense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wace; pakuti wakunga Ine ndani? adzandiikira nthawi ndani? ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?

45. Cifukwa cace tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babulo; ndi zimene walingirira dziko la Akasidi; ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.

46. Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babulo, ndipo mpfuu wamveka mwa amitundu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 50