Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 5:9-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kodi sindidzawalanga cifukwa ca zimenezi? ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera cilango mtundu woterewu?

10. Kwerani pa makoma ace nimupasule; koma musatsirize konse; cotsani nthambi zace pakuti siziri za Yehova.

11. Pakuti nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda zinandicitira monyenga kwambiri, ati Yehova.

12. Akana Yehova, ndi kuti, Si ndiye; coipa sicidzatifika ife; sitidzaona kapena lupanga kapena njala;

13. ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; comweco cidzacitidwa ndi iwo.

14. Cifukwa cace Yehova Mulungu wa makamu atero, Cifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.

15. Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutari, inu nyumba ya Israyeli, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene cinenero cace simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.

16. Phodo lao liri ngati manda apululu, onsewo ndiwo olimba.

17. Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako amuna ndi akazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga midzi yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.

18. Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe.

19. Ndipo padzakhala: pamene mudzati, Cifukwa canji Yehova Mulungu wathu aticitira ife zonse izi? ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yacilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko siliri lanu.

20. Nenani ici m'nyumba ya Yakobo, lalikirani m'Yuda, kuti,

21. Tamvanitu ici, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;

22. Kodi simundiopa Ine? ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mcenga cilekaniro ca nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? ndipo ngakhale mafunde ace acita gabvigabvi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.

23. Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nacoka.

24. Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yace; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.

25. Mphulupulu zanu zacotsa zimenezi, ndi zocimwa zanu zakukanitsani inu zinthu zabwino.

26. Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akucha misampha; acha khwekhwe, agwira anthu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 5