Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 49:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Cifukwa canji udzitamandira ndi zigwa, cigwa cako coyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira cuma cace, nati, Adza kwa ine ndani?

5. Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akucokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ace, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osocera.

6. Koma pambuyo pace ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova.

7. Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi m'Temani mulibenso nzeru? kodi uphungu wawathera akucenjera? kodi nzeru zao zatha psiti?

8. Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala m'Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye.

9. Akafika kwa inu akuchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha?

10. Pakuti ndambvula Esau, ndambvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zace zaonongeka, ndi abale ace, ndi anansi ace, ndipo palibe iye.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 49