Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 49:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Koma za kuopsya kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa citunda, ngakhale usanja cisanja cako pamwamba penipeni ngati ciombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.

17. Ndipo Edomu adzakhala cizizwitso; ndipo yense wakupitapo adzazizwa, ndipo adzatsonyera zobvuta zace zonse.

18. Monga m'kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi midzi inzace, ati Yehova, munthu ali yense sadzakhala m'menemo, mwana wa munthu ali yense sadzagona m'menemo.

19. Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wocokera ku Yordano wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amcokere; ndipo ali yense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wace, pakuti wakunga Ine ndani? adzandiikira nthawi ndani? ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?

20. Cifukwa cace tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala m'Temani, ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.

21. Dziko lapansi linthunthumira ndi phokoso Ija kugwa kwao; pali mpfuu, phokoso lace limveka pa Nyanja Yofiira.

22. Taonani, adzafika nadzauluka ngati ciombankhanga, adzatambasulira Boma mapiko ace, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 49