Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 46:19-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Mwana wamkazi iwe wokhala m'Aigupto, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsya, mulibenso wokhalamo.

20. Aigupto ndi ng'ombe ya msoti yosalala; cionongeko cituruka kumpoto cafika, cafika.

21. Ndiponso olipidwa ace ali pakati pace onga ngati ana a ng'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.

22. Mkokomo wace udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo.

23. Adzatema nkhalango yace, ati Yehova, pokhala yosapitika; pakuti acuruka koposa dzombe, ali osawerengeka.

24. Mwana wace wamkazi wa Aigupto adzacitidwa manyazi, adzaperekedwa m'manja a anthu a kumpoto.

25. Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, ati: Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Aigupto, pamodzi ndi milungu yace, ndi mafumu ace; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye;

26. ndipo ndidzawapereka m'manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndi m'manja a atumiki ace; pambuyo pace adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova.

27. Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usacite mantha, iwe Israyeli: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kucokera kutari, ndi mbeu yako ku dziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m'mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye,

28. Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndiri ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi ciweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 46