Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 46:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri akunena za amitundu.

2. Za Aigupto: kunena za nkhondo ya Farao-neko mfumu ya Aigupto, imene inali pa nyanja ya Firate m'Karikemisi, imene anaikantha Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda.

3. Konzani cikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo.

4. Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zacitsulo; tuulani nthungo zanu, bvalani malaya acitsulo.

5. Cifukwa canji ndaciona? aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osaceukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova.

6. Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pa nyanja ya Firate wapunthwa nagwa.

7. Ndani uyu amene auka ngati Nile, madzi ace ogabvira monga nyanja?

8. Aigupto auka ngati Nile, madzi ace agabvira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ace.

9. Kwerani, inu akavalo; citani misala, inu magareta, aturuke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira cikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.

10. Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza cilango, kuti abwezere cilango adani ace; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa nyanja ya Firate.

11. Kwera ku Gileadi, tenga bvunguti, namwali iwe mwana wa Aigupto; wacurukitsa mankhwala cabe; palibe kucira kwako.

12. Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kupfuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.

13. Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo adzafika adzakantha dziko la Aigupto.

14. Nenani m'Aigupto, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.

15. Akulimba ako akokoledwa bwanji? sanaime, cifukwa Yehova anawathamangitsa,

16. Anapunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzace, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, ku dziko la kubadwa kwathu, kucokera ku lupanga lobvutitsa.

17. Ndipo anapfuula kumeneko, Farao mfumu ya Aigupto ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira,

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 46