Za Aigupto: kunena za nkhondo ya Farao-neko mfumu ya Aigupto, imene inali pa nyanja ya Firate m'Karikemisi, imene anaikantha Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda.