Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 44:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Cifukwa canji mucitira miyoyo yanu coipa ici, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense;

8. popeza muutsa mkwiyo wanga ndi nchito ya manja anu, pofukizira milungu yina m'dziko la Aigupto, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale citemberero ndi citonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi?

9. Kodi mwaiwala zoipa za makolo anu, ndi zoipa za mafumu a Yuda, ndi zoipa za akazi ao, ndi zoipa zanu, ndi za akazi anu, zimene anazicita m'dziko la Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu?

10. Sanadzicepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m'cilamulo canga, kapena m'malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu.

11. Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikucitireni inu coipa, ndidule Yuda lonse.

12. Ndipo ndidzatengaotsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Aigupto akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Aigupto adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkuru, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 44