Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 44:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Aigupto, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti,

2. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Mwaona coipa conse cimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa midzi yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe iri bwinja, palibe munthu wokhalamo;

3. cifukwa ca coipa cao anacicita kuutsa naco mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu yina, Imene sanaidziwa, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.

4. Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musacitetu conyansa ici ndidana naco.

5. Koma sanamvera, sanachera khutu lao kuti atembenuke asiye coipa cao, osafukizira milungu yina.

6. Cifukwa cace mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe.

7. Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Cifukwa canji mucitira miyoyo yanu coipa ici, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense;

8. popeza muutsa mkwiyo wanga ndi nchito ya manja anu, pofukizira milungu yina m'dziko la Aigupto, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale citemberero ndi citonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi?

9. Kodi mwaiwala zoipa za makolo anu, ndi zoipa za mafumu a Yuda, ndi zoipa za akazi ao, ndi zoipa zanu, ndi za akazi anu, zimene anazicita m'dziko la Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu?

10. Sanadzicepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m'cilamulo canga, kapena m'malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 44