16. pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Aigupto, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Aigupto; pamenepo mudzafa.
17. Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Aigupto kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku coipa cimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.
18. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Aigupto; ndipo mudzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo; ndipo simudzaonanso malo ano.
19. Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe m'Aigupto; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero.
20. Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzacita.
21. Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamva mau a Yehova Mulungu wanu m'cinthu ciri conse cimene Iye wanditumira ine naco kwa inu.
22. Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi caola, komwe mufuna kukakhalako.