Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 42:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. cifukwa cace mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe m'Aigupto, kukakhala m'menemo;

16. pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Aigupto, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Aigupto; pamenepo mudzafa.

17. Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Aigupto kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku coipa cimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense.

18. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Aigupto; ndipo mudzakhala citukwano, ndi cizizwitso, ndi citemberero, ndi citonzo; ndipo simudzaonanso malo ano.

19. Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe m'Aigupto; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero.

20. Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzacita.

21. Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamva mau a Yehova Mulungu wanu m'cinthu ciri conse cimene Iye wanditumira ine naco kwa inu.

22. Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi caola, komwe mufuna kukakhalako.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 42