Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 41:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo Ismayeli mwana wa Netaniya anaturuka m'Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wace wa Ahikamu.

7. Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mudzi, Ismayeli mwana, wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye.

8. Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismayeli, Musatiphe ife; pakuti tiri ndi cuma cobisika m'mudzi, ca tirigu, ndi ca barele, ndi ca mafuta, ndi ca uci. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao.

9. Ndipo dzenje moponyamo Ismayeli mitembo yonse ya anthu amene anawapha, cifukwa ca Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa cifukwa ca kuopa Raasa mfumu ya Israyeli, lomwelo Ismayeli mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo.

10. Ndipo Ismayeli anatenga ndende otsala onse a anthu okhala m'Mizipa, ana akazi a mfumu, ndi-anthu onse amene anatsala m'Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismayeli mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni.

11. Koma pamene Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe Onse a nkhondo akhala naye, anamva zoipa zonse anazicita Ismayeli mwana wa Netaniya,

12. anatenga anthu onse, nanka kukamenyana ndi Ismayeli mwana wa Netaniya, nampeza pa madzi ambiri a m'Gibeoni.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 41