Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 4:27-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa.

28. Cifukwa cimeneco dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; cifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.

29. Mudzi wonse uthawa m'phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m'nkhalango, adzakwera pamiyala; midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m'menemo.

30. Nanga iwe, udzacita ciani pamene udzafunkhidwa? Ngakhale udzibveka ndi zofiira, ngakhale udzibveka ndi zokometsera zagolidi, ngakhale udzikuzira maso ako ndi kupaka, udzikometsera pacabe; mabwenzi adzakunyoza adzafuna moyo wako.

31. Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wace woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ace, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! pakuti moyo wanga walefuka cifukwa ca ambanda.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 4