Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 32:29-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. ndipo Akasidi, olimbana ndi mudzi uwu, adzafika nadzayatsa mudziwu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa macitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu yina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.

30. Pakuti ana a Israyeli ndi ana a Yuda anacita zoipa zokha zokha pamaso panga ciyambire ubwana wao, pakuti ana a Israyeli anandiputa Ine kokha kokha ndi nchito ya manja ao, ati Yehova.

31. Pakuti mudzi uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiucotse pamaso panga;

32. cifukwa ca zoipa zonse za ana a Israyeli ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu.

33. Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvera kulangizidwa.

34. Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yochedwa dzina langa, kuti aidetse.

35. Ndipo anamanga misanje ya Baala, iri m'cigwaca mwana wace wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao amuna ndi akazi cifukwa ca Moleki; cimene sindinauza, cimene sicinalowa m'mtima mwanga, kuti acite conyansa ici, cocimwitsa Yuda.

36. Cifukwa cace tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babulo ndi lupanga, ndi njala, ndi caola:

37. Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapitikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukuru, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,

38. ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;

39. ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwacitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;

40. ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawacokera kuleka kuwacitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandicokere.

41. Inde, ndidzasekerera iwo kuwacitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.

42. Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa coipa conseci, comweco ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonieza.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 32