Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 31:23-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'midzi yace, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo cilungamo, iwe phiri lopatulika.

24. Ndipo Yuda ndi midzi yace yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta.

25. Pakuti ndakhutidwa mtima wolema, ndadzazanso mtima uli wonse wacisoni.

26. Pamenepo ndinauka, ndinaona; ndipo tulo tanga tinandizunira ine.

27. Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.

28. Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzyala, ati Yehova.

29. Masiku omwewo sadzanenanso, Atate adya mphesa zowawa, ndi mano a ana ayayamira.

30. Koma yense adzafa cifukwa ca mphulupulu yace; yense amene adya mphesa zowawa, mano ace adzayayamira.

31. Taonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya lsrayeli, ndi nyumba ya Yuda;

32. si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwaturutsa m'dziko la Aigupto; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.

33. Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika cilamulo canga m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzacilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;

34. ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wace, ndi yense mbale wace, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira cimo lao.

35. Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ace agabvira; Yehova wa makamu ndi dzina lace:

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 31