Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 3:11-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo Yehova anati kwa ine, Israyeli wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga,

12. Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israyeli wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndiri wacifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya ku nthawi zonse.

13. Koma bvomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvera mau anga, ati Yehova.

14. Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzi mmodzi wa pa mudzi uli wonse, ndi awiri awiri a pa banja liri lonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni;

15. ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.

16. Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kucuruka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la cipangano ca Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzacitanso konse.

17. Pa nthawi yomweyo adzacha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa.

18. Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderana ndi nyumba ya Israyeli, ndipo adzaturuka pamodzi ku dziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 3