Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 28:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzacitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.

10. Pamenepo Hananiya anacotsa gori pa khosi la Yeremiya, nalityola.

11. Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Comweco ndidzatyola gori la Nebukadinezara mfumu ya Babulo zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulicotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anacoka.

12. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, atatyola Hananiya mneneri gori kulicotsa pa khosi la Yeremiya, kuti,

13. Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Watyola magori amtengo; koma udzapanga m'malo mwao magori acitsulo.

14. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ndaika gori lacitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama za kuthengo.

15. Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutuma iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama.

16. Cifukwa cace Yehova atero, Taona, Ine ndidzakucotsa iwe kudziko; caka cino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.

17. Ndipo anafa Hananiya caka comweco mwezi wacisanu ndi ciwiri.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 28