Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 28:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi maufumu akuru, za nkhondo, ndi za coipa, ndi za caola.

9. Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzacitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.

10. Pamenepo Hananiya anacotsa gori pa khosi la Yeremiya, nalityola.

11. Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Comweco ndidzatyola gori la Nebukadinezara mfumu ya Babulo zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulicotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anacoka.

12. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, atatyola Hananiya mneneri gori kulicotsa pa khosi la Yeremiya, kuti,

13. Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Watyola magori amtengo; koma udzapanga m'malo mwao magori acitsulo.

14. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ndaika gori lacitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama za kuthengo.

15. Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutuma iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama.

16. Cifukwa cace Yehova atero, Taona, Ine ndidzakucotsa iwe kudziko; caka cino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.

17. Ndipo anafa Hananiya caka comweco mwezi wacisanu ndi ciwiri.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 28