Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 27:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,

2. Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magori, nuziike pakhosi pako;

3. nuzitumize kwa mfumu ya Edomu, ndi kwa mfumu ya Moabu, ndi kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kwa mfumu ya Turo, ndi kwa mfumu ya Zidoni, ndi dzanja la amithenga amene afika ku Yerusalemu kwa Zedekiya mfumu ya Yuda;

4. nuwauze iwo anene kwa ambuyao, kuti, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Muzitero kwa ambuyanu:

5. Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikuru ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.

6. Tsopano ndapereka maiko onse awa m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga; ndiponso nyama za kuthengo ndampatsa iye kuti zimtumikire.

7. Ndipo amitundu, onse adzamtumikira iye, ndi mwana wace, ndi mdzukulu wace, mpaka yafika nthawi ya dziko lace; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu akuru adzamuyesa iye mtumiki wao.

8. Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babulo, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi caola, mpaka nditatha onse ndi dzanja lace.

9. Koma inu, musamvere aneneri anu, kapena akuombeza anu, kapena maloto anu, kapena alauli anu, kapena obwebweta anu, Musadzatumikira mfumu ya ku Babulo;

10. kakuti iwo akunenerani inu zonama, kuti akucotseni inu m'dziko lanu, kunka kutari kuti ndikupitikitseni inu, ndipo inu mudzathedwa.

11. Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa gori la mfumu ya ku Babulo, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.

12. Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'gori la mfumu ya ku Babulo, ndi kumtumikira iye ndi anthu ace, ndipo mudzakhala ndi moyo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 27