Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 25:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndico caka coyamba ca Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo;

2. amene Yeremiya ananena kwa anthu onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu, kuti:

3. Kuyambira caka cakhumi ndi citatu ca Yosiya mwana wace wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero lomwe, zakazi makumi awiri ndi zitatu, mau a Yehova anafika kwa ine, ndipo ndanena kwa inu, pouka mamawa ndi kunona; koma simunamvera.

4. Ndipo Yehova watuma kwa inu atumiki ace onse ndiwo aneneri, pouka mamawa ndi kuwatuma; koma simunamvera, simunachera khutu lanu kuti mumve;

5. ndi kuti, Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yace yoipa, ndi zoipa za nchito zanu, ndi kukhala m'dziko limene Yehova anapatsa inu ndi makolo anu, kuyambira kale kufikira muyaya;

6. musatsate milungu yina kuitumikira, ndi kuigwadira, musautse mkwiyo wanga ndi nchito ya manja anu; ndingacitire inu coipa.

7. Koma simunandimvera Ine, ati Yehova; kuti muutse mkwiyo wanga ndi nchito ya manja anu ndi kuonapo coipa inu.

8. Cifukwa cace Yehova wa makamu atero: Popeza simunamvera mau anga,

9. taonani, Ine ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo pa dziko lino, ndi pa okhalamo ace onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo cizizwitso, ndi cotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.

10. Ndiponso ndidzawacotsera mau akusekera ndi mau akukondwera, ndi mau a mkwati, ndi mau a mkwatibwi, mau a mphero, ndi kuwala kwa nyali.

11. Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi cizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka makumi asanu ndi awiri.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 25