Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 23:9-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; cifukwa ca Yehova, ndi cifukwa ca mau ace opatulika.

10. Pakuti dziko ladzala ndi acigololo; pakuti cifukwa ca temberero dziko lilira, mabusa a kucipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siiri yabwino.

11. Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.

12. Cifukwa cace njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzacotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, caka ca kulangidwa kwao, ati Yehova.

13. Ndipo ndinaona kupusa mwa aneneri a ku Samariya; anenera za Baala, nasokeretsa anthu anga Israyeli.

14. Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona cinthu coopsetsa; acita cigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ocita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zace; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ace ngati Gomora.

15. Cifukwa cace Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo cowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwaturukira kunka ku dziko lonse.

16. Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zacabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.

17. Anena cinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wace amati, Palibe coipa cidzagwera inu.

18. Pakuti ndani waima m'upo wa Yehova, kuti aone namve mau ace? ndani wazindikira mau anga, nawamva?

19. Taonani, cimphepo ca Yehova, kupsa mtima kwace, kwaturuka, inde cimphepo cozungulira; cidzagwa pamutu pa woipa.

20. Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atacita, mpaka atatha maganizo a mtima wace; masiku otsiriza mudzacidziwa bwino.

21. Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanena ndi iwo, koma ananenera.

22. Koma akadaima m'upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo ku njira yao yoipa, ndi ku coipa ca nchito zao.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 23