Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 17:8-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuti madzi, wotambalitsa mizu yace pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lace likhala laliwisi; ndipo subvutika cakaca cirala, suleka kubala zipatso.

9. Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosaciritsika, ndani angathe kuudziwa?

10. Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa imso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zace, monga zipatso za nchito zace.

11. Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikira, momwemo iye amene asonkhanitsa cuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ace cidzamsiya iye, ndipo pa citsirizo adzakhala wopusa.

12. Malo opatulika athu ndiwo mpando wacifumu wa ulemerero, wokhazikika pamsanje ciyambire.

13. Inu Yehova, ciyembekezo ca Israyeli, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondicokera Ine adzalembedwa m'dothi, cifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.

14. Mundiciritse ine, Yehova, ndipo ndidzaciritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti cilemekezo canga ndinu.

15. Taonani, ati kwa ine, Mau a Yehova ali kuti? adze tsopano.

16. Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumira kucokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumba tsiku la tsoka; Inu mudziwa, cimene cinaturuka pa milomo yanga cinali pamaso panu.

17. Musakhale wondiopsetsa ine; ndinu pothawira panga tsiku la coipa.

18. Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la coipa, muwaononge ndi cionongeko cowirikiza.

19. Yehova anatero kwa ine: Pita, nuime m'cipata ca ana a anthu, m'mene alowamo mafumu a Yuda, ndi m'mene aturukamo, ndi m'zipata zonse za Yerusalemu;

20. ndipo uziti kwa iwo, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi Ayuda onse, ndi onse okhala m'Yerusalemu, amene alowa pa zipatazi;

21. atero Yehova: Tadziyang'anirani nokha, musanyamule katundu tsiku la Sabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu;

22. musaturutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire nchito iri onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;

23. koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve, asalandire langizo.

24. Ndipo padzakhala, ngati mu ndimveretsa Ine, ati Yehova, kuti musalowetse katundu pa zipata za mudzi uwu tsiku la Sabata, koma mupatule tsiku la Sabata, osagwira nchito m'menemo;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 17