Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 16:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndiponso mau a Mulungu anadza kwa ine, kuti,

2. Usatenge mkazi, usakhale ndi ana amuna ndi akazi m'malo muno.

3. Pakuti Yehova atero za ana amuna ndi za ana akazi akubadwa m'malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m'dziko muno:

4. Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala cakudya ca mbalame za kumlengalenga, ndi zirombo za dziko lapansi.

5. Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukacita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndacotsa mtendere wanga pa anthu awa, cifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.

6. Akuru ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzacita maliro ao, sadzadziceka, sadzadziyeseza adazi, cifukwa ca iwo;

7. anthu sadzawagawira mkate pamaliro, kuti atonthoze mitima yao cifukwa ca akufa, anthu sadzapatsa iwo cikho ca kutonthoza kuti acimwe cifukwa ca atate ao kapena mai wao.

8. Usalowe m'nyumba ya madyerero kukhala nao, ndi kudya ndi kumwa.

9. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 16