Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 14:11-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino.

12. Pamene asala cakudya, sindidzamva kupfuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi cirala, ndi caola.

13. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi cirala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.

14. Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi cinthu cacabe, ndi cinyengo ca mtima wao.

15. Cifukwa cace atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatuma, koma ati, Lupanga ndi cirala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi cirala aneneriwo adzathedwa.

16. Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu cifukwa ca cirala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna ndi akazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 14