Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 13:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

9. Yehova atero, Momwemo ndidzaononga kudzitama kwa Yuda, ndi kudzitama kwakukuru kwa Yerusalemu.

10. Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu yina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.

11. Pakuti monga mpango uthina m'cuuno ca munthu, comweco ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israyeli ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi cilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.

12. Cifukwa cace uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo?

13. Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi ciledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala m'Yerusalemu.

14. Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi cisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi cifundo, cakuti ndisawaononge.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 13