Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 12:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; cifukwa canji ipindula njira ya oipa? cifukwa canji akhala bwino onyengetsa?

2. Inu mwabzyala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patari ndi imso zao.

3. Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwaturutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.

4. Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? cifukwa ca zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona citsiriziro cathu.

5. Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akavalo bwanji? ndipo ngakhale ukhazikika m'dziko lamtendere, udzacita ciani m'kudzikuza kwa Yordano?

6. Pakuti ngakhale abale ako, ndi nyumba ya atate wako, ngakhale iwo anakunyenga iwe; ngakhale anakupfuulira iwe; usamvere iwo, ngakhale anena nawe mau abwino.

7. Ndacokaku nyumba yanga, ndasiya colowa canga; ndapereka wokondedwa wa mtima wanga m'dzanja la adani.

8. Colowa canga candisandukira mkango wa m'nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ace; cifukwa cace ndinamuda.

9. Colowa canga ciri kwa ine ngati mbalame yamawala-mawala yolusa? kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? mukani, musonkhanitse zirombo za m'thengo, mudze nazo zidye.

10. Abusa ambiri aononga munda wanga wamphesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa cipululu copanda kanthu.

11. Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; cifukwa palibe munthu wosamalira.

12. Akufunkha afika pa mapiri oti se m'cipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali yina ya dziko kufikira ku mbali yina; palibe thupi lokhala ndi mtendere.

13. Abzyala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, cifukwa ca mkwiyo woopsya wa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 12