Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? cifukwa ca zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona citsiriziro cathu.