Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 10:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo cilangizo, copanda pace.

9. Abwera ndi siliva wa ku Tarisi, wosulasula wopyapyala ndi golidi wa ku Ufazi, nchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zobvala zao ndi nsaru ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi nci ito za muomba.

10. Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wace dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wace.

11. Muzitero nao, milungu imene sinalenga miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha ku dziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo.

12. Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yace, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yace, nayala thambo ndi kuzindikira kwace;

13. polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, naturutsa mphepo m'zosungira zace.

14. Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lace losemasema; pakuti fanizo lace loyenga liri bodza, mulibe mpweya mwa iwo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 10