Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 4:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Nati Boazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmoabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa colowa cace.

6. Ndipo woombolerayo anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge colowa canga; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.

7. Koma kale m'Israyeli pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu abvula nsapato yace, naipereka kwa mnansi wace; ndiwo matsimikizidwe m'Israyeli.

8. Ndipo woombolayo anati kwa Boazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Nabvula nsapato yace.

9. Nati Boazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, pa dzanja la Naomi.

10. Ndiponso Rute Mmoabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa colowa cace; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ace, ndi pa cipata ca malo ace; inu ndinu mboni lero lino.

11. Pamenepo anthu onse anali kucipata, ndi akuru, anati, Tiri mboni ife. Yehova acite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israyeli, iwo awiri; nucite iwe moyenera m'Efrata, numveke m'Betelehemu;

Werengani mutu wathunthu Rute 4