Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 2:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Potero anagwa nkhope yace pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima cifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?

11. Ndipo Boazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unacitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi mako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.

12. Yehova akubwezere nchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israyeli, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ace.

13. Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena cokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu.

14. Ndipo pa nthawi ya kudya Boazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m'vinyo wosasayo. Nakhala iye m'mbali mwa ocekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo.

15. Ndipo ataumirira kukatola khunkha, Boazi analamulira anyamata ace ndi kuti, Atole khunkha ngakhale pakati pa mitolo, musamcititse manyazi.

16. Ndiponso mumtayire za m'manja, ndi kuzisiya, natole khunkha, osamdzudzula.

17. Natola khunka iye m'munda mpaka madzulo; naomba khunkhalo napeza ngati licero la barele,

18. nalisenza nalowa kumudzi; ndipo mpongozi wace anaona khunkhalo; Rute naturutsanso nampatsa mkute uja anausiya atakhuta.

19. Ndipo mpongozi wace ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? ndi nchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wace munthu amene anakagwirako nchito, nati, Dzina lace la munthuyo ndinakagwirako nchito lero ndiye Boazi.

20. Nati Naomi kwa mpongozi wace, Yehova amdalitse amene sanaleka kuwacitira zokoma amoyo, ndi akufa. Ndipo Naomi ananena baye, Munthuyu ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera colowa.

Werengani mutu wathunthu Rute 2