Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 22:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo, namanga mahema m'zigwa za Moabu, tsidya la Yordano ku Yeriko.

2. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anaona zonse Israyeli anacitira Aamori.

3. Ndipo Moabu anacita mantha akuru ndi anthuwo, popeza anacuruka; nada mtima Moabu cifukwa ca ana a Israyeli.

4. Ndipo Moabu anati kwa akuru a Midyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse ziri pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Moabu masiku amenewo.

5. Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wace, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anaturuka anthu m'dziko la Aigupto; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.

6. Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawalaka, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapitikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.

7. Ndipo akuru a Moabu ndi akuru a Midyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.

Werengani mutu wathunthu Numeri 22