Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 11:6-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. koma tsopano moyo wathu waphwa; tiribe kanthu pamaso pathu koma mana awa.

7. Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ace ngati maonekedwe a bedola.

8. Anthu amamka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.

9. Ndipo pakugwa mame pacigono usiku, mana anagwapo.

10. Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wace; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.

11. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Munacitiranji coipa mtumiki wanu? ndalekeranii kupeza ufulu pamaso panu, kuti muika pa ine katundu wa anthu awa onse?

12. Kodi ndinaima nao anthu awa onse? kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kumka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao?

13. Ndidzaiona kuti nyama yakuwapatsa anthu awa onse? pakuti amalirira ine, ndi kuti, Tipatseni nyama, tidye.

14. Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine.

15. Ndipo ngati mundicitira cotero, mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang'ane tsoka langa.

16. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akuru a Israyeli, amene uwadziwa kuti ndiwo akuru a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku cihema cokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.

17. Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uti pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha.

18. Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m'makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? popeza tinakhala bwino m'Aigupto, Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya.

19. Simudzadya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku asanu, kapena masiku khumi, kapena masiku makumi awiri;

20. koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pace, ndi kuti, Tinaturukiranji m'Aigupto?

21. Ndipo Mose anati, Anthu amene ndiri pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu.

22. Kodi adzawaphera magulu a nkhosa ndi ng'ombe, kuwakwanira? kapena kodi nsomba zonse za m'nyanja zidzawasonkhanira pamodzi, kuwakwanira?

23. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? tsopano udzapenya ngati mau anga adzakucitikira kapena iai.

24. Ndipo Mose anaturuka, nauza anthu mau a Yehova; nasonkhanitsa akuru a anthu makumi asanu ndi awiri, nawaimika pozungulira pa cihema.

Werengani mutu wathunthu Numeri 11