Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uti pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha.