Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 9:29-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. ndipo munawacitira umboni, kuti muwabwezerenso ku cilamulo canu; koma anacita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anacimwira malamulo anu (amene munthu akawacita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.

30. Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwacitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvera; cifukwa cace munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko.

31. Ndipo mwa nsoni zanu zocuruka simunawatha, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa cisomo ndi cifundo.

32. Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkuru, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi cifundo, asacepe pamaso panu mabvuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akuru athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asuri, mpaka lero lino.

33. Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwacita zoona, koma ife tacita coipa;

34. ndi mafumu athu, akuru athu, ansembe athu, ndi makolo athu, sanasunga cilamulo canu, kapena kumvera malamulo anu, ndi mboni zanu, zimene munawacitira umboni nazo.

35. Popeza sanatumikira Inu m'ufumu wao, ndi m'ubwino wanu wocuruka umene mudawapatsa, ndi m'dziko lalikuru ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerera kuleka nchito zao zoipa.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 9