Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 9:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israyeli anasonkhana ndi kusala, ndi kubvala ciguduli, ndipo anali ndi pfumbi.

2. Nadzipatula a mbumba ya Israyeli kwa alendo onse, naimirira, naulula zocimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.

3. Naimima poima pao, nawerenga m'buku la cilamulo ca Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anaulula, napembedza Yehova Mulungu wao.

4. Pamenepo anaimirira pa ciunda ca Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyeli, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, napfuula ndi mau akuru kwa Yehova Mulungu wao.

5. Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyeli, Buni, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petatiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu ku nthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa cilemekezo ndi ciyamiko conse.

6. Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse ziri pomwepo, nyanja ndi zonse ziri m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu la kumwamba lilambira Inu.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 9