Naimima poima pao, nawerenga m'buku la cilamulo ca Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anaulula, napembedza Yehova Mulungu wao.