Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 8:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Nawerenga iwo m'buku m'cilamulo ca Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa cowerengedwaco.

9. Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamacita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a cilamulo.

10. Nanena naonso, Mukani mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lace iye amene sanamkonze ratu kanthu; cifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamacita cisoni; pakuti cimwemwe ca Yehova ndico mphamvu yanu.

11. Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli cete; pakuti lero ndi lopatulika; musamacita cisoni.

12. Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukuru; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera.

13. Ndipo m'mawa mwace akuru a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a cilamulo.

14. Napeza munalembedwa m'cilamulo kuti Yehova analamulira ndi Mose, kuti ana a Israyeli azikhala m'misasa pa madyerero a mwezi wacisanu ndi ciwiri,

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 8