Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 5:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndinatinso, Cinthu mucitaci si cokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, cifukwa ca mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?

10. Kodi ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, tiwakongoletsa ndarama ndi tirigu mwa phindu? Ndikupemphani, tileke phindu ili.

11. Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao yaazitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndarama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.

12. Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzacita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzacita monga mwa mau awa.

13. Ndinakutumulanso maraya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, ku nyumba yace, ndi ku nchito yace; inde amkutumule momwemo, namtayire zace zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anacita monga mwa mau awa.

14. Ndipo ciyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira caka ca makumi awiri kufikira caka ca makumi atatu mphambu ziwiri ca Aritasasta mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadya cakudya ca kazembe.

15. Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakale anyamata ao anacita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, cifukwa ca kuopa Mulungu.

16. Ndiponso ndinalimbikira nchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligula, ndi anyamata anga onse anasonkhanira nchito komweko.

17. Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi; mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kucokera kwa amitundu otizinga.

18. Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundu mitundu; cinkana conseci sindinafunsira cakudya ca kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo.

19. Mundikumbukire Mulungu, zindikomere zonse ndinacitira anthu awa.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 5