Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 3:15-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndi cipata ca kukasupe anacikonza Saluni mwana wa Koli, Hoze mkuru wa dziko la Mizipa anacimanga, nacikomaniza pamwamba pace, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace; ndiponso linga la dziwe la Sela pa munda wa mfumu, ndi kufikira ku makwerero otsikira ku mudzi wa Davide.

16. Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkuru wa dera lace lina la dziko la Bete Zuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi ku nyumba ya amphamvu aja.

17. Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pace anakonza Hasabiya mkuru wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lace.

18. Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkuru wa dera lina la dziko la Keila.

19. Ndi pa mbali pace Ezeri mwana wa Yesuwa, mkuru wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera ku nyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga.

20. Potsatizana naye Baruki mwana wa Zabai anafulumira kukonza gawo lina kuyambira popindirira mpaka ku khomo la nyumba ya Eliasibu mkuru wa ansembe.

21. Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uliya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira ku khomo la nyumba ya Eliasibu kufikira malekezero ace a nyumba ya Eliasibu.

22. Ndi potsatizana naye anakonza ansembe okhala kucidikha.

23. Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubi pandunji pa nyumba pao, Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maseya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yace.

24. Potsatizana naye Binui mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira ku nyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungondya.

25. Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene iri ku bwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.

26. Koma Anetini okhala m'Ofeli anakonza kufikira ku malo a pandunji pa cipata ca kumadzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo,

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 3