Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 3:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafi, pandunji pa nyumba yace. Ndi pambali pace anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya.

11. Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubi mwana wa Pahati-Moabu, anakonzal gawo lina, ndi nsanja ya ng'anjo.

12. Ndi pambali pace anakonza Salumu mwana wa Halohesi, mkuru wa dera lina la dziko la Yerusalemu, iye ndi ana ace akazi.

13. Cipata ca kucigwa anacikonza Hanini; ndi okhala m'Zanowa anacimanga, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace; ndiponso mikono cikwi cimodzi ca lingalo mpaka ku cipata ca kudzala.

14. Ndi cipata ca kudzala anacikonza Malikiya mwana wa Rekabu, mkuru wa dziko la Bete Hakeremu; anacimanga, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace.

15. Ndi cipata ca kukasupe anacikonza Saluni mwana wa Koli, Hoze mkuru wa dziko la Mizipa anacimanga, nacikomaniza pamwamba pace, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace; ndiponso linga la dziwe la Sela pa munda wa mfumu, ndi kufikira ku makwerero otsikira ku mudzi wa Davide.

16. Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkuru wa dera lace lina la dziko la Bete Zuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi ku nyumba ya amphamvu aja.

17. Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pace anakonza Hasabiya mkuru wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lace.

18. Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkuru wa dera lina la dziko la Keila.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 3