Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Ngakhale Mulungu apatsa munthu zonse azikhumba koma mtima sukhuta nazo

1. Pali coipa ndaciona kunja kuno cifalikira mwa anthu,

2. munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa cuma ndi ulemu, mtima wace susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ici ndi cabe ndi nthenda yoipa,

3. Cinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zace ndi kucuruka, koma mtima wace osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;

4. pakuti ikudza mwacabe, nicoka mumdima, mdima nukwirira dzina lace.

5. Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;

6. akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita ku malo amodzi?

7. Nchito zace zonse munthu angogwirira m'kamwa mwace, koma mtima wace sukhuta.

8. Pakuti wanzeru ali ndi ciani coposa citsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pa maso pa amoyo ali ndi ciani?

9. Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.

10. Comwe cinalipo cachedwa dzina lace kale, cidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu.

11. Pokhala zinthu zambiri zingocurukitsa zacabe, kodi anthu aona phindu lanji?

12. Pakuti ndani adziwa comwe ciri cabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wace wacabe umene autsiriza ngati mthunzi? pakuti ndani adzauza munthu cimene cidzaoneka m'tsogolo mwace kunja kuno?