Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 1 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Za pansi pano nzacabe

1. MAU a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya m'Yerusalemu.

2. Zacabecabe, ati Mlaliki; zacabecabe zonse ndi cabe.

3. Kodi nchito zace zonse munthu asauka nazo zimpindulira ciani?

4. Mbadwo wina opita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse,

5. inde dzuwa lituruka, nililowa, nilifulumira komwe linaturukako.

6. Kulowa kumwela ndi kuzungulira: kumpoto zungulire zungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ace.

7. Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.

8. Zinthu zonse zilemetsa; munthu sakhoza kuzifotokoza; maso sakhuta m'kuona, ndi makutu sakhuta m'kumva.

9. Comwe cinaoneka cidzaonekanso; ndi comwe cinacitidwa cidzacitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano.

10. Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.

11. Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zirinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.

12. Ine Mlaliki ndinali mfumu ya: Israyeli m'Yerusalemu.

13. Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimacitidwa pansi pa thambo; nchito yobvuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.

14. Ndaona nchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi cabe ndi kungosautsa mtima.

15. Cokhotakhota sicingaongokenso; ndipo coperewera sicingawerengedwe.

16. Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi cidziwitso.

17. Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti icinso cingosautsa mtima.

18. Pakuti m'nzeru yambiri muli cisoni cambiri; ndi yemwe aenjezera cidziwitso aenjezera zowawa.