Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Tizicita zokoma lero lino posadziwa za mawa

1. Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.

2. Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa coipa canji cidzaoneka pansi pano.

3. Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwela pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo.

4. Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.

5. Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa nchito za Mulungu amene acita zonse.

6. Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino.

7. Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa.

8. Inde, munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo; koma akumbukire masiku amdima kuti adzacuruka. Zonse zirinkudza ziri zacabe.

Anyamata asangalale, koma adzikonzeretu pokumbukira imfa ikudza

9. Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.

10. Cifukwa cace cotsani zopweteka m'mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa cabe.