Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mika 4:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma kudzacitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.

2. Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zace, ndipo tidzayenda m'mabande ace; pakuti ku Ziyoni kudzaturuka cilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.

3. Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzace lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.

4. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wace, ndi patsinde pa mkuyu wace; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.

5. Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mlungu wace, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthawi yomka muyaya.

6. Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzamemeza wakutsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopitikitsidwayo, ndi iye amene ndinamsautsa;

Werengani mutu wathunthu Mika 4